[Civsoc-mw] Malamulo a Mpira Tili Ana

Tony Thontholani tonytontho at yahoo.com
Tue Oct 1 22:48:57 CAT 2019


Wolemba: KLK
———————•
MALAMULO AMPIRA TILI ANA
1. Aliyense onenepa amakhala pa golo.!!
2. Mwini wake wa mpira amasankha timu
yosewera.
3. Penate imabwera ngati ovulala walira.
4. Mpira umatha aliyense akatopa.
5. Ngati sunathandize nawo kukhonza
mpira sumamenya nawo.
6. Sipamakhala oyimbira.
7. Yemwe sanasankhidwe nawo kumenya
amakhala bolera.
8. Mwini mpira akakwiya mpira umathera
pompo.
9. Ukaputhwa mumpira mankhwala ake
limakhala dothi.
10. Wina akamakana kutulutsidwa
amakhala nyama.(a timu inayo
amauzidwa
kuti azimponda).
11. Mwini wake wampira samatulutsidwa
olo akhale osatha kuopa kuti kuti atenga
mpira wake.
12. Ukakhala wamkulu sumamenya
nawo.
13. Makona kick akakwana 5
motsogozana
imakhala penate.
14. Sipakhala offside.
15. Ukaponda mwini mpira umatulutsidwa.
16. Golo boy ngati sayeza mpira wa
mmwamba chimakhala chigoli.
17. Mwini wake wa mpira akamuyitana
kwawo mpira umathera pompo.
18. Panalibe kuyendera nthawi.
Timayendera zigoli; 2 change 2 watha.
19. Mpira umayamba player odalilika
akafika. Ngati wachedwa mumamudikira.
20. Mwini wa mpira akatopa mpira
umathera pompo.
Kale timanjoya ndithu.
21. lifali amakondela timu yochokela
kwawo
kuopa kumumenya popita

-- 
This message has been scanned for viruses and
dangerous content by MailScanner, and is
believed to be clean.




More information about the Civsoc-mw mailing list